1 Akorinto 4:1-21

4  Chotero anthu azitha kuona kuti ndife atumiki+ a Khristu ndi oyang’anira+ zinsinsi zopatulika+ za Mulungu.  Komanso pamenepa, chofunika kwa woyang’anira+ ndicho kukhala wokhulupirika.+  Tsopano zonena kuti ndiweruzidwe ndi inu kapena ndi bwalo lina lililonse la anthu+ si nkhani kwa ine. Ngakhale ine ndemwe sindidziweruza ndekha.  Pakuti sindikudziwa+ kanthu kalikonse konditsutsa mumtima mwanga. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti basi ndine wolungama, koma Yehova ndiye amandifufuza.+  Chotero musaweruze+ kalikonse nthawi isanakwane, mpaka Ambuye adzafike.+ Akadzafika adzaunika zinsinsi za mu mdima+ ndi kuonetsa poyera+ zolingalira za m’mitima, ndipo aliyense adzatamandidwa yekha ndi Mulungu.+  Tsopano abale, zinthu zimenezi ndazinena monga zochitika kwa ine mwini ndi Apolo+ kuti inuyo mupindule, kuti muphunzire kwa ife lamulo ili lakuti: “Musapitirire zinthu zolembedwa,”+ kuti aliyense wa inu asadzitukumule+ pokonda munthu wina n’kudana ndi wina.+  Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana+ ndi ena ndani? Inde, uli ndi chiyani chimene sunachite kulandira?+ Ndiye ngati unachita kulandira zinthu zimenezo,+ n’chifukwa chiyani ukudzitama+ ngati kuti sunachite kulandira?  Kodi anthu inu mwakhuta kale eti? Mwalemera kale, si choncho?+ Kodi mwayamba kale kulamulira monga mafumu+ popanda ife? Ndikanakondadi mukanayamba kulamulira monga mafumu, kuti ifenso tilamulire limodzi nanu monga mafumu.+  Pakuti ndikuona ngati Mulungu waika atumwife kukhala ngati omalizira pachionetsero+ monga anthu okaphedwa,+ chifukwa takhala ngati choonetsedwa m’bwalo la masewera+ kudziko, kwa angelo,+ ndi kwa anthu.+ 10  Takhala opusa+ chifukwa cha Khristu, koma inu mwakhala ochenjera+ mwa Khristu. Ife ndife ofooka,+ inu ndinu amphamvu.+ Inu muli ndi mbiri yabwino,+ koma ifeyo tikunyozedwa.+ 11  Mpaka pano tikadali anjala+ ndi aludzu+ ndi ausiwa.+ Tikuzunzidwabe,+ tikusowabe pokhala,+ 12  ndipo tikugwirabe ntchito yolimba+ ndi manja athu.+ Pamene akutinenera zachipongwe, timadalitsa.+ Pozunzidwa, timapirira.+ 13  Ponyozedwa, timayankha mofatsa.+ Mpaka tsopano, takhala ngati zinyalala za dziko, nyansi za zinthu zonse.+ 14  Sikuti ndikulemba zinthu zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni monga ana anga okondedwa.+ 15  Pakuti ngakhale mutakhala ndi aphunzitsi+ 10,000 mwa Khristu, ndithudi mulibe abambo ambiri,+ pakuti mwa Khristu Yesu ndakhala bambo anu kudzera mwa uthenga wabwino.+ 16  Chotero ndikukuchondererani, tsanzirani ineyo.+ 17  Ndiye chifukwa chake ndikukutumizirani Timoteyo,+ popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika+ mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimachitira zinthu potumikira Khristu Yesu,+ monga mmenenso ineyo ndikuphunzitsira kulikonse, mumpingo uliwonse. 18  Ena amadzitukumula+ ngati kuti sindidzabwera n’komwe kwanuko. 19  Koma ndifika kwanuko posachedwapa, Yehova akalola,+ ndipo sindidzafuna kumva mawu a odzitukumulawo, koma ndidzafuna ndione mphamvu yawo. 20  Pakuti ufumu wa Mulungu sunagone m’mawu, koma mu mphamvu.+ 21  Kodi mukufuna chiyani? Mukufuna ndibwere kwa inu ndi chikwapu,+ kapena ndi chikondi ndi mzimu wofatsa?+

Mawu a M'munsi