1 Akorinto 3:1-23

3  Chotero abale, sindinathe kulankhula nanu monga anthu auzimu,+ koma monga anthu oganiza ngati anthu a m’dzikoli,* monga tiana+ mwa Khristu.  Ndinakupatsani mkaka, osati chakudya chotafuna,+ chifukwa munali musanalimbe mokwanira. Komatu ngakhale tsopano simunalimbebe mokwanira,+  chifukwa mukadali anthu oganiza ngati anthu a m’dzikoli.*+ Kodi ngati mukuchitirana nsanje ndi kukangana nokhanokha,+ sindiye kuti ndinu akuthupi ndipo mukuyenda monga anthu?+  Ngati wina akunena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ndipo wina akunenanso kuti: “Ine ndine wa Apolo,”+ kodi sindiye kuti mukungofanana ndi anthu onse basi?  Kodi Apolo ndani?+ Inde, Paulo ndani? Iwo angokhala atumiki+ amene anakuthandizani kukhala okhulupirira, malinga ndi ntchito imene Ambuye anagawira aliyense wa iwo.  Ineyo ndinabzala,+ Apolo anathirira,+ koma Mulungu ndiye anakulitsa.+  Chotero wobzala+ kapena wothirira sali kanthu, koma Mulungu amene amakulitsa.+  Choncho wobzala ndi wothirira ali amodzi,+ koma aliyense payekha adzalandira mphoto yake mogwirizana ndi ntchito yake.+  Pakuti ndife antchito anzake a Mulungu.+ Inuyo ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa,+ nyumba ya Mulungu.+ 10  Malinga ndi kukoma mtima kwakukulu+ kumene Mulungu anandisonyeza, ndinayala maziko+ monga woyang’anira wanzeru wa ntchito zomangamanga, koma amene akumanga pamaziko amenewo ndi munthu wina. Aliyense asamale mmene akumangirapo.+ 11  Pakuti palibe munthu wina amene angayale maziko ena+ alionse kupatulapo amene anayalidwawo, omwe ndi Yesu Khristu.+ 12  Tsopano ngati munthu akumanga pamazikowo ndi golide, siliva, miyala yamtengo wapatali, mitengo, udzu ndi ziputu, 13  ntchito ya wina aliyense idzaonekera. Pakuti tsikulo lidzasonyeza ntchitoyo poyera, chifukwa moto ndiwo udzaonetsa zimenezo poyera,+ ndipo motowo udzaonetsa kuti ntchito ya munthu aliyense ndi yotani. 14  Ngati ntchito imene munthu wamanga pamazikowo idzakhalapobe,+ iye adzalandira mphoto.+ 15  Ngati ntchito ya munthu idzatenthedwa ndi moto, ndiye kuti zake zatayika, koma iyeyo adzapulumuka.+ Koma ngakhale adzatero, adzakhala ngati wapulumuka pamoto.+ 16  Kodi inu simukudziwa kuti ndinu kachisi wa Mulungu,+ ndi kuti mzimu wa Mulungu ukukhala mwa inu?+ 17  Ngati munthu aliyense wawononga kachisi wa Mulungu, Mulungu adzawononganso munthu ameneyo,+ pakuti kachisi wa Mulungu ndi woyera,+ ndipo kachisiyo+ ndinuyo.+ 18  Munthu asamadzinyenge yekha: Ngati aliyense wa inu akudziyesa wanzeru+ mu nthawi* ino, akhale wopusa kuti akhale wanzeru.+ 19  Pakuti kwa Mulungu nzeru za m’dzikoli n’zopusa,+ chifukwa Malemba amati: “Iye amakola anzeru m’kuchenjera kwawo.”+ 20  Ndiponso: “Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu anzeru ndi opanda pake.”+ 21  Chotero pasakhale munthu wodzitama chifukwa cha anthu, popeza zinthu zonse ndi zanu,+ 22  kaya Paulo, Apolo,+ Kefa, dziko, moyo, imfa, zinthu zimene zilipo tsopano kapena zimene zidzakhalapo,+ zonse ndi zanu. 23  Inuyo ndinu ake a Khristu,+ ndipo Khristu ndi wa Mulungu.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “anthu akuthupi.”
Mawu ake enieni, “anthu akuthupi.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.