1 Akorinto 14:1-40

14  Yesetsani kukhala ndi chikondi, komanso pitirizani kufunafuna mwachangu mphatso zauzimu,+ makamaka kunenera.+  Chifukwa wolankhula lilime lachilendo salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu, pakuti palibe amene amamva zonena zake,+ koma amalankhula zinsinsi zopatulika+ mwa mzimu.  Komabe, wonenera amathandiza+ anthu ndipo amawalimbikitsa ndi kuwatonthoza ndi mawu ake.  Wolankhula lilime lachilendo amadzilimbikitsa yekha, koma wonenera amalimbikitsa mpingo.  Tsopano ndikanakonda kuti nonsenu muzilankhula malilime,+ koma ndikuona kuti ndi bwino kuti muzinenera.+ Ndithudi, wonenera amaposa wolankhula malilime achilendo,+ kupatulapo ngati wa malilimeyo amasulira, kuti amange mpingo.  Koma pa nthawi ino abale, ngati ineyo ndingabwere kwa inu ndikulankhula malilime, kodi mungapindulepo chiyani ngati sindingakulankhuleni ndi mawu amene ndalandira kuchokera kwa Mulungu,+ kapena ndi mphatso yodziwa zinthu,+ kapena ndi ulosi, kapena ndi chiphunzitso?  Chabwino, zinthu zopanda moyo zimamveka kulira kwake,+ kaya chikhale chitoliro kapena zeze. Koma ngati maliridwe ake angokhala amodzi osasinthasintha, kodi n’zotheka kudziwa nyimbo imene ikuimbidwa ndi chitoliro kapena zezeyo?  Ndithudi, ngati lipenga likulira mwa mamvekedwe osadziwika bwino, ndani angakonzekere nkhondo?+  Momwemonso, ngati simukulankhula zomveka ndi lilime lanu,+ zingatheke bwanji kudziwa zimene mukunena? Kwenikweni mudzakhala mukulankhula kwa mphepo.+ 10  Pangakhale zinenero zosiyanasiyana padziko lapansi, koma palibe zinenero zimene zilibe tanthauzo. 11  Chotero ngati sindikudziwa tanthauzo la chinenero, ndimakhala mlendo+ kwa wolankhulayo, ndipo wolankhulayo amakhala mlendo kwa ine. 12  Inunso chimodzimodzi, popeza mukufunitsitsa mphatso za mzimu.+ Chotero, yesetsani kukhala nazo zochuluka kuti mumange mpingo.+ 13  Choncho amene amalankhula lilime lachilendo apemphere kuti athe kumasulira.+ 14  Pakuti ngati ndikupemphera m’lilime lachilendo, mphatso yanga ya mzimu ndi imene ikupemphera,+ koma maganizo anga amakhala opanda phindu. 15  Ndiye chofunika n’chiyani? Ndipemphere ndi mphatso ya mzimu, koma ndipempherenso ndi maganizo anga. Ndiimbe chitamando ndi mphatso ya mzimu,+ koma ndiimbenso ndi maganizo anga.+ 16  Chifukwa ngati mupereka chitamando ndi mphatso ya mzimu, kodi munthu wamba anganene bwanji “Ame”+ pa kuyamika kwanu, posadziwa zimene mukunena? 17  Zoonadi, mukupereka chiyamiko m’njira yabwino, koma munthu winayo sakulimbikitsidwa.+ 18  Ndimayamika Mulungu kuti ndimalankhula malilime ambiri kuposa nonsenu.+ 19  Ngakhale zili choncho, ndi bwino kuti mumpingo ndilankhule mawu asanu omveka, kutinso ndilangize ena ndi mawuwo, kusiyana n’kulankhula mawu 10,000 m’lilime lachilendo.+ 20  Abale, musakhale ana aang’ono pa luntha la kuzindikira,+ koma khalani tiana pa zoipa,+ ndipo pa luntha la kuzindikira khalani aakulu msinkhu.+ 21  M’Chilamulo muli mawu akuti: “‘Anthu awa+ ndidzawalankhula m’malilime a alendo,+ ndipo ndidzawalankhula ndi milomo ya anthu achilendo, koma iwo sadzandimverabe,’ watero Yehova.”+ 22  Chotero malilimewo ndi chizindikiro+ kwa osakhulupirira,+ osati kwa okhulupirira, koma kunenera ndi kwa okhulupirira,+ osati osakhulupirira. 23  Ndiye chifukwa chake, ngati mpingo wonse wasonkhana malo amodzi ndipo onse akulankhula malilime,+ ndiyeno mwalowa anthu osadziwa kalikonse kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti ndinu amisala? 24  Koma ngati nonse mukunenera, ndiyeno mwalowa winawake wosakhulupirira kapena munthu wamba, iye amadzudzulidwa ndi nonsenu.+ Nonsenu mumamufufuza mosamala. 25  Zobisika za mumtima mwake zimaululika,+ moti adzagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi, n’kulambira Mulungu, ndi kunena kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.”+ 26  Ndiyeno zizikhala bwanji, abale? Mukasonkhana pamodzi, wina amakhala ndi salimo, wina chiphunzitso, wina mawu amene walandira kuchokera kwa Mulungu, wina lilime lachilendo, wina kumasulira.+ Zochitika zonse zikhale zolimbikitsa.+ 27  Ndipo ngati pali anthu olankhula lilime lachilendo, asapose awiri kapena atatu, azisiyirana mpata, ndipo wina amasulire.+ 28  Koma ngati palibe womasulira, wa malilimeyo akhale chete mumpingo. Adzilankhule yekha mumtima+ ndipo alankhule kwa Mulungu. 29  Aneneri awiri kapena atatu+ alankhule, ndipo ena onse azindikire tanthauzo la zimene iwo alankhula.+ 30  Koma ngati mneneri wina amene wakhala pansi walandira mawu kuchokera kwa Mulungu,+ woyambayo akhale chete. 31  Pakuti nonse munganenere,+ koma mmodzi ndi mmodzi, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa.+ 32  Ndipo mphatso za mzimu za aneneri ziyenera kulamulidwa ndi aneneri. 33  Pakuti Mulungu si Mulungu wachisokonezo,+ koma wamtendere.+ Mofanana ndi m’mipingo yonse ya oyerawo, 34  akazi akhale chete+ m’mipingo, pakuti sikololeka kuti iwo azilankhula, koma akhale ogonjera,+ monga Chilamulo+ chimanenera. 35  Koma ngati akufuna kumvetsa chinachake, akafunse amuna awo kunyumba, popeza n’zochititsa manyazi+ kuti mkazi azilankhula mumpingo. 36  Kodi mawu a Mulungu anachokera kwa inu,+ kapena anafika kwa inu nokha? 37  Ngati munthu akuganiza kuti ndi mneneri kapena ali ndi mphatso ya mzimu, avomereze zimene ndakulemberanizi, chifukwa ndizo lamulo la Ambuye.+ 38  Koma ngati wina savomereza, akhale. 39  Choncho abale anga, pitirizani kufunafuna mwakhama uneneri,+ komanso musaletse kulankhula malilime.+ 40  Koma zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.+

Mawu a M'munsi