1 Akorinto 13:1-13

13  Ngati ndimalankhula malilime+ a anthu ndi a angelo koma ndilibe chikondi, ndakhala ngati belu longolira, kapena chinganga chosokosera.+  Ndipo ngati ndili ndi mphatso yonenera,+ yodziwa zinsinsi zonse zopatulika,+ yodziwa zinthu zonse,+ komanso ngati ndili ndi chikhulupiriro chonse choti n’kusuntha nacho mapiri,+ koma ndilibe chikondi, sindili kanthu.+  Ngati ndapereka zanga zonse kudyetsa ena,+ ndipo ngati ndapereka thupi langa+ kuti ndidzitame, koma ndilibe chikondi,+ sindinapindule m’pang’ono pomwe.  Chikondi+ n’choleza mtima+ ndiponso n’chokoma mtima.+ Chikondi sichichita nsanje,+ sichidzitama,+ sichidzikuza,+  sichichita zosayenera,+ sichisamala zofuna zake zokha,+ sichikwiya.+ Sichisunga zifukwa.+  Sichikondwera ndi zosalungama,+ koma chimakondwera ndi choonadi.+  Chimakwirira zinthu zonse,+ chimakhulupirira zinthu zonse,+ chimayembekezera zinthu zonse,+ chimapirira zinthu zonse.+  Chikondi sichitha.+ Koma kaya pali mphatso za kunenera, zidzatha. Kaya kulankhula malilime, kudzatha. Ngakhale mphatso ya kudziwa zinthu, idzatha.+  Pakuti tikudziwa+ moperewera ndipo tikunenera mopereweranso.+ 10  Koma chokwanira chikadzafika,+ choperewerachi chidzatha. 11  Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, ndiponso kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula,+ ndasiya zachibwana. 12  Pakuti pa nthawi ino sitikuona bwinobwino chifukwa tikugwiritsa ntchito galasi losaoneka bwinobwino,+ koma pa nthawiyo zidzakhala maso ndi maso.+ Pa nthawi ino zimene ndikudziwa n’zoperewera, koma pa nthawiyo ndidzadziwa bwinobwino ngati mmene ineyo ndikudziwikira bwinobwino.+ 13  Komabe, tsopano patsala zitatu izi: Chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.+

Mawu a M'munsi