1 Akorinto 11:1-34

11  Muzitsanzira ine, monga mmene inenso ndimatsanzirira Khristu.+  Tsopano ndikukuyamikirani chifukwa chakuti mukundikumbukira m’zinthu zonse, ndipo mukusunga miyambo+ monga mmene ndinaiperekera kwa inu.  Koma ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.+ Mutu wa mkazi ndi mwamuna,+ ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.+  Mwamuna aliyense amene akupemphera kapena kunenera atavala chinachake kumutu akuchititsa manyazi mutu wake,+  koma mkazi aliyense amene akupemphera kapena kunenera+ osavala kanthu kumutu akuchititsa manyazi mutu wake,+ popeza n’chimodzimodzi ndi kumeta mpala.+  Ngati mkazi savala kanthu kumutu, amete mpala, koma ngati zili zochititsa manyazi kuti mkazi amete kwambiri tsitsi lake kapena amete mpala,+ azivala chakumutu.+  Mwamuna sayenera kuphimba kumutu kwake, popeza iye ndi chifaniziro+ ndi ulemerero+ wa Mulungu, koma mkazi ndi ulemerero wa mwamuna.+  Pakuti mwamuna sanachokere kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna,+  ndiponso mwamuna sanalengedwere mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna.+ 10  Ndiye chifukwa chake mkazi ayenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro kumutu kwake+ chifukwa cha angelo.+ 11  Ndiponso mwa Ambuye, mkazi sakhalapo popanda mwamuna kapena mwamuna popanda mkazi.+ 12  Pakuti monga mkazi ali wochokera kwa mwamuna,+ mwamunanso amakhalapo kudzera mwa mkazi,+ koma zinthu zonse ndi zochokera kwa Mulungu.+ 13  Weruzani nokha: Kodi n’koyenera mkazi kupemphera kwa Mulungu osaphimba kumutu? 14  Kodi chikhalidwe sichikuphunzitsani kuti ngati mwamuna ali ndi tsitsi lalitali, zimenezi n’zochititsa manyazi kwa iye, 15  koma ngati mkazi ali ndi tsitsi lalitali, ndi ulemerero kwa iye?+ Zili choncho chifukwa wapatsidwa tsitsi lakelo m’malo mwa chovala kumutu.+ 16  Komabe, ngati alipo wina amene akuoneka kuti akutsutsa+ zimenezi pofuna chikhalidwe china,+ ifeyo, monganso mipingo ya Mulungu, tilibe chikhalidwe chinanso. 17  Koma pamene ndikupereka malangizo awa, sikuti ndikukuyamikirani ayi, chifukwa mukasonkhana pamodzi, simusonkhanira zabwino, koma zoipa.+ 18  Choyamba, mukasonkhana mumpingo, ndamva kuti pamachitika magawano pakati panu,+ ndipo m’mbali zina ndikukhulupirira kuti zimenezi ndi zoona. 19  Pakuti payeneradi kukhala magulu ampatuko+ pakati panu, kuti anthu ovomerezedwa aonekere pakati panu.+ 20  Chotero, mukasonkhana pamalo amodzi, sizitheka kudya chakudya chamadzulo cha Ambuye moyenerera.+ 21  Pakuti, mukamadya, aliyense amakhala atadya chakudya chake chamadzulo, choncho wina amakhala ndi njala koma wina amakhala woledzera. 22  Zoona, kodi mulibe nyumba zimene mungadyeremo ndi kumweramo?+ Kapena kodi mukunyoza mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi anthu amene alibe kalikonse?+ Kodi ndinene chiyani kwa inu? Ndikuyamikireni? Koma pa izi zokha sindingakuyamikireni. 23  Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye n’zimene inenso ndinakupatsirani, zakuti Ambuye Yesu, usiku+ umene anali kukaperekedwa anatenga mkate. 24  Ndipo atayamika, anaunyemanyema+ n’kunena kuti: “Mkate uwu ukuimira thupi langa+ limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.”+ 25  Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu+ atadya chakudya chamadzulo, ndipo anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano+ pamaziko a magazi anga.+ Muzichita zimenezi nthawi zonse pamene mukumwa za m’kapu imeneyi pondikumbukira.”+ 26  Pakuti nthawi zonse+ pamene mukudya mkate umenewu ndi kumwa za m’kapu imeneyi, mukulengezabe imfa+ ya Ambuye, mpaka iye adzafike.+ 27  Ndiye chifukwa chake aliyense wakudya mkatewu kapena kumwa za m’kapu ya Ambuye mosayenerera, adzakhala ndi mlandu+ wokhudza thupi ndi magazi+ a Ambuye. 28  Munthu ayambe wadzifufuza+ ngati ali woyenerera kudya mkatewu ndi kumwa za m’kapuyi. 29  Pakuti munthu wakudya ndi kumwa, akudya ndi kumwa chilango+ chake ngati sazindikira thupilo. 30  Ndiye chifukwa chake ambiri mwa inu ali ofooka ndi odwaladwala, ndipo angapo akugona+ mu imfa. 31  Koma ngati tingazindikire mmene tilili, sitingaweruzidwe.+ 32  Komabe tikaweruzidwa,+ ndiye kuti taphunzitsidwa ndi Yehova+ kuti tisalandire chilango+ pamodzi ndi dziko.+ 33  Choncho abale anga, mukasonkhana pamodzi kuti mudye chakudya chamadzulo cha Ambuye,+ dikiranani. 34  Ngati wina ali ndi njala, adye kunyumba,+ kuti musasonkhanire kuweruzidwa.+ Koma nkhani zotsalazo ndidzathana nazo ndikadzafika komweko.

Mawu a M'munsi