1 Akorinto 10:1-33

10  Tsopano sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale, kuti makolo athu akale, onse anali pansi pa mtambo+ ndipo onse anawoloka nyanja.+  Onse anabatizidwa mwa Mose,+ kudzera mwa mtambo ndi mwa nyanja.  Ndiponso, onse anadya chakudya chimodzimodzi chauzimu,+  ndipo onse anamwa chakumwa chimodzimodzi chauzimu.+ Pakuti anali kumwa pathanthwe lauzimu+ limene linali kuwatsatira, ndipo thanthwelo+ linatanthauza Khristu.+  Ngakhale zinali choncho, ambiri a iwo Mulungu sanakondwere+ nawo, ndipo anathana+ nawo m’chipululu.  Tsopano zinthu zimenezi zinakhala zitsanzo kwa ife, kuti ifenso tisakhale anthu olakalaka zinthu zoipa+ ngati mmene iwo anachitira.  Ndipo tisapembedze mafano, mmene ena mwa iwo anachitira,+ monga mmene Malemba amanenera kuti: “Anthu anakhala pansi ndi kudya ndiponso kumwa. Kenako anaimirira n’kuyamba kusangalala.”+  Tisamachite dama,+ mmene ena mwa iwo anachitira dama, n’kufa 23,000 tsiku limodzi.+  Kapena tisamuyese Yehova,+ mmene ena mwa iwo anamuyesera,+ n’kuwonongeka polumidwa ndi njoka.+ 10  Tisakhalenso ong’ung’udza, mmene ena mwa iwo anang’ung’udzira,+ wowonongayo+ n’kuwawononga onsewo. 11  Tsopano zinthu zimenezi zinali kuwagwera monga zitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze+ ifeyo amene mapeto a nthawi* zino atifikira.+ 12  N’chifukwa chake amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.+ 13  Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene amagwera anthu ena.+ Koma Mulungu ndi wokhulupirika+ ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire,+ koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira+ kuti muthe kuwapirira. 14  Ndiye chifukwa chake, okondedwa anga, thawani+ kupembedza mafano.+ 15  Ndikulankhula nanu ngati anthu ozindikira.+ Dziwani nokha zimene ndikunena. 16  Kodi kapu+ ya dalitso imene timadalitsa, sitanthauza kugawana magazi a Khristu?+ Kodi mkate umene timanyema,+ sutanthauza kugawana thupi la Khristu? 17  Popeza pali mkate umodzi, ifeyo, ngakhale kuti tilipo ambiri,+ ndife thupi limodzi,+ pakuti tonse tikudya nawo mkate umodziwo.+ 18  Taganizirani zochitika za Isiraeli wakuthupi:+ Kodi amene amadyako zoperekedwa nsembe sindiye kuti akugawana ndi guwa lansembe?+ 19  Ndiye ndinene chiyani? Kuti choperekedwa nsembe kwa fano chili kanthu, kapena kuti fanolo ndi kanthu?+ 20  Ayi, koma ndikunena kuti zinthu zimene mitundu ina imapereka nsembe imazipereka kwa ziwanda,+ osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti mukhale ogawana ndi ziwanda.+ 21  Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova*+ komanso za m’kapu ya ziwanda. Sizingatheke kuti muzidya “patebulo la Yehova”+ komanso patebulo la ziwanda. 22  Kapena “kodi tikufuna kuputa nsanje+ ya Yehova”? Kodi mphamvu zathu zingafanane ndi zake?+ 23  Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zaphindu.+ Zinthu zonse ndi zololeka,+ koma si zonse zimene zili zolimbikitsa.+ 24  Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi,+ koma zopindulitsanso wina.+ 25  Chilichonse chogulitsidwa pamsika wa nyama muzidya+ popanda kufunsa mafunso, poopera chikumbumtima+ chanu, 26  chifukwa “dziko lapansi ndi zonse za mmenemo+ ndi za Yehova.”+ 27  Ngati wina mwa osakhulupirira wakuitanani ndipo mwapita, kadyeni zonse zimene wakupatsani,+ popanda kufunsa mafunso poopera chikumbumtima chanu.+ 28  Koma wina akakuuzani kuti: “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo poopera amene wakuuzaniyo ndiponso poopera chikumbumtima.+ 29  Sindikunena “chikumbumtima” chako koma cha munthu winayo. N’chifukwa chiyani ufulu wanga ukulamulidwa ndi chikumbumtima cha munthu wina?+ 30  Ngati ndikudya chakudyacho nditayamika Mulungu, kodi ndinyozedwe pa chinthu chimene ndayamikira?+ 31  Ndiye chifukwa chake, kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.+ 32  Pewani kukhala okhumudwitsa+ kwa Ayuda, ngakhalenso kwa Agiriki, ndi kwa mpingo wa Mulungu, 33  monga mmene ineyo ndikukondweretsera anthu onse m’zinthu zonse.+ Sikuti ndikungofuna zopindulitsa ine ndekha ayi,+ koma zopindulitsa anthu ambiri, kuti apulumutsidwe.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 2.